Khansala Abdullah Yusuf kuchokera kudera la Mangochi Makanjira, lero amusankha kukhala wapampando watsopano wa Khonsolo ya Mangochi.Yusuf yemwe ndiwachipani cha Democratic Progressive (DPP) wagonjetsa yemwe anali paudindowu Hassan Chikuta wachipani cha Malawi Congress (MCP) ndimavoti 24 kwa 11.
Imran Nyambi oimira dera la Chilipa ndiyemwe wasankhidwa ngati wachiwiri kwa Abdullah Yusuf. Masankhowa achitikira ku Wapansi Hotel m’boma la Mangochi. Pachisankhochi panali aphungu komanso makhansala 35 omwe pamodzi akupanga Khonsolo ya Mangochi.