• Wed. Oct 16th, 2024

NICE ilimbikitsa mgwirizano polimbikitsa amayi, achinyamata kutengapo gawo pa masankho a mu 2025

Bungwe lophunzitsa ndi kuzindikiritsa anthu pa zinthu zosiyanasiyana la National Initiative for Civic Education (NIC) lamema okhudzidwa onse kuti agwirana manja pa ntchito yolimbikitsa amayi ndi achinyamata kutengapo gawo pa masankho a mchaka chamawa.

Mkulu wa bungweli a Gray Kalindekafe ndi amene adapereka pempholi m’boma la Dedza masiku apitawa pamene amakhazikitsidwa ngati Katswiri Wachimuna (Male Champion) wa 50-50 Kampeni.

A Kalindekafe (achinayi kuchokera kumanzere) ndi akuluakulu ena pa mwambowo

Mwambowu udachitika pamodzi ndi mwambo wokhazikitsa ndondomeko ya Political Empowerment of Women (PEW) m’bomali.

A Kalindekafe anati ndi zochititsa chisoni ndi manyazi kuti amayi akupitirira kuponderezedwa ngakhale kuti pali malamulo owateteza ku nkhanza za mtundu wina uliwonse.

“Kwanthawi yayitali, amayi akhala akusalidwa panthawi yomwe pakuperekedwa ziganizo za ndale. Komabe tikudziwa kuti amayi akpatsidwa mpata nkulimbikitsidwa kuti liwu lawo limveke, amabweretsa mfundo zachilendo komanso zothandiza kupereka upangiri wabwino pazokambirana. Amayi ndiwo tsinde la mmakomo athu ndipo utsogoleri wawo ndi wofunika pobweretsa dziko la chilungamo ndi losakondera,” adatero mkuluyu.

Pa mwambowu padafika akuluakulu a mabungwe osiyanasiyana monga la European Union (EU), lomwe limaperekanso thandizo ku NICE, komanso Centre for Civil Society Strengthening (CCSS) komanso phungu wa ku Nyumba ya Malamulo a Joshua Malango ndi akuluakulu ena ochokera ku boma.

A Kalindekafe anati ndondomeko ya PEW ndi chiyambi chofunikira kwambiri kuti Malawi akwaniritse masomphenya olimbikitsa amayi.

Iwo anafotokoza kuti cholinga chachikulu cha PEW ndiye ndi kupititsa patsogolo dongosolo lakuti amayi, achinyamata ndi aulumali asamasiyidwe kunja koma azitenga nawo mbali mmakomiti osiyanasiyana komanso pa zoganizo zosiyanasiyana.

“Ndondomeko imeneyi yitenga magawo angapo monga nkhani ya zamalamulo ndi ndondomeko za kayendetsedwe ka zinthu (legal and policy frameworks), malamulo oyendetsera zipani (Political party regulations) ndinso kulimbikitsa kuti amayi azidzidalira pa kapezedwe ka chuma (women’s economic empowerment). Ngati zimenezi zingatheke, zingabweretse kusintha kwakukulu pa momwe ndale zathu zikuyendera muno m’Malawi,” iwo anatero.

“Choncho tiyeni tigwirane manja pothetsa zonse zomwe zingalepheretse amayi kutenga nawo mbali pa ndale. Tikatero tithandiza kuti dziko lathu lipite patsogolo pozindikira kuti akachita bwino mzimayi, tonse tidzachita bwino,” adapempha chotere mkuluyu.

Author

By admin

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *